Psalms 49

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

1Imvani izi anthu a mitundu yonse;
mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,
2anthu wamba pamodzi ndi anthu odziwika,
olemera pamodzinso ndi osauka:
3Pakamwa panga padzayankhula mawu anzeru;
mawu ochokera mu mtima mwanga adzapereka nzeru.
4Ndidzatchera khutu langa ku mwambo,
ndi pangwe ndidzafotokoza momveka mwambi wanga.

5Ine ndichitirenji mantha pamene masiku oyipa afika,
pamene achinyengo oyipa andizungulira.
6Iwo amene adalira kulemera kwawo
ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo?
7Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake
kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu.
8Dipo la moyo ndi la mtengowapatali,
palibe malipiro amene angakwanire,
9kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya
ndi kusapita ku manda.

10Pakuti onse amaona kuti anthu anzeru amamwalira;
opusa ndi opanda nzeru chimodzimodzinso amawonongeka
ndipo amasiyira chuma chawo anthu ena.
11Manda awo adzakhala nyumba zawo mpaka muyaya,
malo awo okhalako kwa nthawi yonse ya mibado yawo,
ngakhale anatchula malo mayina awo.

12Ngakhale munthu akhale wachuma chotani,
adzafa ngati nyama.

13Izi ndi zimene zimachitikira iwo amene amadzidalira okha,
ndi owatsatira awo amene amavomereza zimene amayankhula.
Sela
14Monga nkhosa iwo ayenera kupita ku manda,
ndipo imfa idzawadya.
Olungama adzawalamulira mmawa;
matupi awo adzavunda mʼmanda,
kutali ndi nyumba zawo zaufumu.
15Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda;
ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.

16Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera,
pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;
17Pakuti sadzatenga kanthu pamodzi naye pamene wamwalira,
ulemerero wake sudzapita pamodzi naye.
18Ngakhale pamene munthuyo ali moyo amadziyesa wodala,
ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino,
19iyeyo adzakakhala pamodzi ndi mʼbado wa makolo ake,
amene sadzaonanso kuwala.

20Munthu amene ali ndi chuma koma wopanda nzeru
adzafa ngati nyama yakuthengo.
Copyright information for NyaCCL